Kalata kwa Dr. Joyce Banda

download

The Elections that has created horros in Malawi

(Copied)

Wokondeka Mayi Joyce Banda,

Ndamvetsedwa kuti muli ku London kumene adakuyitanani a BBC kuti mukalankhule ndi azimayi amzanu. Zosangalatsa tu zimenezo mayi. Zimenezi zangotiwonetsera a Malawi kuti muja timakunenani kuti mukuwononga ndalama za boma kamba koyendayenda inu simumawononga ndalama zoyi chifukwa apa kuyenda mukuyendaku nanga mukugwiritsa ntchito ndalama zaboma?

Mayi Banda inu m’mene mumatuluka mboma munasiya Dollar Kwacha ili pa K375 koma m’mene ndikulemba kalatamu, kuti ugule 1 dollar paufunika K520. Muikhululukire timakunyozani kuti Kwacha ikugwa chifukwa ndinu a Mandasi, koma ayi ndithu ikugwabe ngakhale pa mpando pali pulofesa. Moti ife pano nkhawa biii kuti pofika chaka cha m’mawa I dollar ikhala ili pa bwanji.

Tikakamba za shuga ndiye hmmm ayi zosautsa. Mumakheta mwathumu pa shop tikugula K650. pajatu inu m’mene mumatuluka Shuga adali pa K450 koma pano tikukhulupilira kuti shuga ameneyu afika K1000.

Tikukamba ndi chisoni podziwa kuti tinakamba zambiri zokunyozani zomwe zina sizimakukhuzani a President. Tinkanena ife kuti mbava zikukudelerani chifukwa ndinu mzimayi. Komatu ngakhale analowa awawa amati athetsa umbava wa zinthu ndiye zikunkera nkera kuvuta mayi Joyce Banda. Nyamata oyimba uyu Maovololo wawomebledwa dzulo dzuloli. Driver wa ku Agriculture yemwe waphedwa ndi zigawenga pofuna kuba galimoto, nduyu tayika lero kuu Ntcheu. Anthu akungopedwa ngati nkhuku mdziko muno, koma izi zikuchitika pali aja amati akudziwa amene amapanga za umbava. hmmm takulirani masiteni.

Dandaulo lathu kwambiri liri pa a First Lady. A City amatilemba ntchito mbuyo mu yosesa komanso kuwola zinyalala ndikumatipatsa ka change potha pa mwezi kuti tikadye ndi family kunyumba. Koma pano a First lady akuti adayambitsa bungwe lomwe likumasesa komanso kuwola zinyalala ndipo ife a City sakufuna nso kutileba ntchito.

Tinalonjezedwa kuti ma salary akwera. Ndipo ma salary wo adakweradi, koma anakwezera mabwana okha ndi 100%. Ma Principal Secretary omwe amalandia kale zindalama zambiri adawakwezela ndi 100%, ma Director chimodzimodzi koma ife a ma change anangotipatsa 47% yokha. Kungotipaka nsuzi a President akale inu.

Ma Blackberry timayenda nawo ku ma shiner pa town aja pano tu a Airtel anasintha ma charges moti Blackberry tidapachika pano. It is an unaffordable to have a blackberry ndithu mayi. Ukakhala uyu timamuti Airtel money ndiye sakugwilika, akungotibera basi.

National team ija akuti bai isasewerenso ma game otsala kamba kakuti ndalama palibe. Zoseketsa kwambiri ndithu mayi tikaganiza kuti pulofesa adatenga anthu 68 kupita nao ku America uko kutali mkumatiuza kuti ndalama zotengera anthu 20 kupita nawo pa Ethiopia pompa apa kulibe. Taziwona ndikuzigwira ife.

Hahahaha zina kuti tikambe apa masiteni tikhala ngati tikuwonjeza koma khulupilirani ndithu. A police asiye kugwira akuba pano ntchito yawo akumawotcha misika akuti. Akuba avuta mu ma location mu, kuba ma battery a galimoto osati pang’ono. Kunja kwawopsa uku.

Onena mkumati ndiye moyowo koma moyo wanji otere. Mimoto yosayamba. Pano tingodikila kuti kupsanso ndikuti. Kapena zija anatilonjeza mu manifesto kuti moto buuuuu zinali zowona tu? Ambuye akusamalireni Mayi Joyce Banda. Kuthekera kwanu takudziwa tsopano. Ife tili pano kulirira kuwutsi kudikila kuti fuel akweza liti, ma coupon tilandira liti, ndipo dollar ifika pa bwanji?

Mukamabwera ku UK ko mutigulire jersey ya Chelsea yolemba DROGBA kumbuyo.

Zikomo

Ndatha Ine Wanu Wodandaula,
Mofolo Ndaganiza Chomwera Phiri
Blantyre